17. Ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhiraA mvunja ndi cisiyo ndi mtanthanyerere.
18. Tiye tikondwere ndi cikondano mpaka mamawa;Tidzisangalatse ndi ciyanjano.
19. Pakuti mwamuna kulibe kwathu,Wapita ulendo wa kutari;
20. Watenga thumba la ndalama m'dzanja lace,Tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.
21. Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ace,Ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yace.
22. Mnyamatayo amtsata posacedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa;Ndi monga unyolo umadza kulanga citsiru;
23. Mpaka mubvi ukapyoza mphafa yace;Amtsata monga mbalame yotamangira msampha;Osadziwa kuti adzaononga moyo wace.
24. Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,Labadirani mau a m'kamwa mwanga.
25. Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo,Usasocere m'mayendedwe ace.
26. Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa;Ndipo ophedwa ndi iye acurukadi.
27. Nyumba yace ndiyo njira ya kumanda,Yotsikira ku zipinda za imfa.