Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 7:15-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Cifukwa cace ndaturuka kudzakucingamira,Kudzafunitsa nkhope yako, ndipo ndakupeza.

16. Ndayala zopfunda pakama panga,Nsaru zamangamanga za thonje la ku Aigupto,

17. Ndakapiza pamphasa panga mankhwala onunkhiraA mvunja ndi cisiyo ndi mtanthanyerere.

18. Tiye tikondwere ndi cikondano mpaka mamawa;Tidzisangalatse ndi ciyanjano.

19. Pakuti mwamuna kulibe kwathu,Wapita ulendo wa kutari;

20. Watenga thumba la ndalama m'dzanja lace,Tsiku lowala mwezi adzabwera kwathu.

21. Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ace,Ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yace.

22. Mnyamatayo amtsata posacedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa;Ndi monga unyolo umadza kulanga citsiru;

23. Mpaka mubvi ukapyoza mphafa yace;Amtsata monga mbalame yotamangira msampha;Osadziwa kuti adzaononga moyo wace.

24. Ndipo tsopano, ananga, mundimvere ine,Labadirani mau a m'kamwa mwanga.

25. Mtima wako usapatukire ku njira ya mkaziyo,Usasocere m'mayendedwe ace.

26. Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa;Ndipo ophedwa ndi iye acurukadi.

27. Nyumba yace ndiyo njira ya kumanda,Yotsikira ku zipinda za imfa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 7