Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 7:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwananga, sunga mau anga,Ukundike malangizo anga;

2. Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo;Ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.

3. Uwamange pa zala zako,Uwalembe pamtima pako;

4. Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongwanga;Nuche luntha mbale wako.

5. Kuti zikucinjirizire kwa mkazi waciwerewere,Kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ace.

6. Pakuti pa zenera la nyumba yangaNdinapenyera pa made ace;Ndinaona pakati pa acibwana,

7. Ndinazindikira pakati pa ang'onoMnyamata wopanda nzeru,

8. Alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo,Ndi kuyenda pa njira ya ku nyumba yace;

9. Pa madzulo kuli sisiro,Pakati pa usiku pali mdima,

10. Ndipo taona, mkaziyo anamcingamira,Atabvala zadama wocenjera mtima,

11. Ali wolongolola ndi wosaweruzika,Mapazi ace samakhala m'nyumba mwace.

12. Mwina ali kumakwalala, mwina ali kumabwalo,Nabisalira pa mphambano zonse.

13. Ndipo anagwira mnyamatayo, nampsompsona;Nati kwa iye ndi nkhope yacipongwe,

Werengani mutu wathunthu Miyambi 7