1. Mwananga, sunga mau anga,Ukundike malangizo anga;
2. Sunga malangizo anga, nukhale ndi moyo;Ndi malamulo anga ngati mwana wa diso lako.
3. Uwamange pa zala zako,Uwalembe pamtima pako;
4. Nena kwa nzeru, Ndiwe mlongwanga;Nuche luntha mbale wako.
5. Kuti zikucinjirizire kwa mkazi waciwerewere,Kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ace.
6. Pakuti pa zenera la nyumba yangaNdinapenyera pa made ace;Ndinaona pakati pa acibwana,
7. Ndinazindikira pakati pa ang'onoMnyamata wopanda nzeru,
8. Alikupita pakhwalala pafupi ndi mphambano ya pa mkaziyo,Ndi kuyenda pa njira ya ku nyumba yace;
9. Pa madzulo kuli sisiro,Pakati pa usiku pali mdima,
10. Ndipo taona, mkaziyo anamcingamira,Atabvala zadama wocenjera mtima,