6. Pita kunyerere, wolesi iwe,Penya njira zao nucenjere;
7. Ziribe mfumu,Ngakhale kapitao, ngakhale mkuru;
8. Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe;Nizituta dzinthu zao m'masika.
9. Udzagona mpaka liti, wolesi iwe?Udzauka ku tulo tako liti?
10. Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono,Kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;
11. Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.
12. Munthu wopanda pace, mwamuna wamphulupulu;Amayenda ndi m'kamwa mokhota;
13. Amatsinzinira ndi maso ace, napalasira ndi mapazi ace,Amalankhula ndi zala zace;
14. Zopotoka ziri m'mtima mwace, amaganizira zoipa osaleka;Amapikisanitsa anthu.
15. Cifukwa cace tsoka lace lidzadza modzidzimuka;Adzasweka msanga msanga, palibe compulumutsa.
16. Ziripo zinthu zisanu ndi cimodzi Mulungu azida;Ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:
17. Maso akunyada, lilime lonama,Ndi manja akupha anthu osacimwa;
18. Mtima woganizira ziwembu zoipa,Mapazi akuthamangira mphulupulu mmangu mmangu;
19. Mboni yonama yonong'ona mabodza,Ndi wopikisanitsa abale.
20. Mwananga, sunga malangizo a atate wako,Usasiye malamulo a mako;
21. Uwamange pamtima pako osaleka;Uwalunze pakhosi pako.
22. Adzakutsogolera ulikuyenda,Ndi kukudikira uli m'tulo,Ndi kulankhula nawe utauka.
23. Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika;Ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo;
24. Zikucinjiriza kwa mkazi woipa,Ndi ku lilime losyasyalika la mkazi waciwerewere.
25. Asakucititse kaso m'mtima mwako,Asakukole ndi zikope zace.