Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 6:29-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Comweco wolowa kwa mkazi wa mnzace;Womkhudzayo sadzapulumuka cilango.

30. Anthu sanyoza mbala ikaba,Kuti ikhutitse mtima wace pomva njala;

31. Koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri;Idzapereka cuma conse ca m'nyumba yace.

32. Wocita cigololo ndi mkazi alibe nzeru;Wofuna kuononga moyo wace wace ndiye amatero.

33. Adzalasidwa nanyozedwa;Citonzo cace sicidzafafanizidwa.

34. Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna,Ndipo sadzacitira cifundo tsiku lobwezera cilango.

35. Sadzalabadira ciombolo ciri conse,Sadzapembedzeka ngakhale ucurukitsa malipo,

Werengani mutu wathunthu Miyambi 6