Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 6:24-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Zikucinjiriza kwa mkazi woipa,Ndi ku lilime losyasyalika la mkazi waciwerewere.

25. Asakucititse kaso m'mtima mwako,Asakukole ndi zikope zace.

26. Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamariza ndi nyenyeswa;Ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatari.

27. Kodi mwamuna angatenge moto pa cifuwa cace,Osatentha zobvala zace?

28. Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka,Osapsya mapazi ace?

29. Comweco wolowa kwa mkazi wa mnzace;Womkhudzayo sadzapulumuka cilango.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 6