Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 6:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mwananga, ngati waperekera mnzako cikole,Ngati wapangana kulipirira mlendo,

2. Wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako,Wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.

3. Cita ici tsono; mwananga, nudzipulumutse;Popeza walowa m'dzanja la mnzako,Pita nudzicepetse, numdandaulire mnzako,

4. Usaone tulo m'maso mwako,Ngakhale kuodzera zikope zako.

5. Dzipulumutse wekha ngati mphoyo ku dzanja la msaki,Ndi mbalame ku dzanja la msodzi.

6. Pita kunyerere, wolesi iwe,Penya njira zao nucenjere;

7. Ziribe mfumu,Ngakhale kapitao, ngakhale mkuru;

8. Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe;Nizituta dzinthu zao m'masika.

9. Udzagona mpaka liti, wolesi iwe?Udzauka ku tulo tako liti?

10. Tulo ta pang'ono, kuodzera pang'ono,Kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;

11. Ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,Ndi kusauka kwako ngati munthu wacikopa.

12. Munthu wopanda pace, mwamuna wamphulupulu;Amayenda ndi m'kamwa mokhota;

13. Amatsinzinira ndi maso ace, napalasira ndi mapazi ace,Amalankhula ndi zala zace;

Werengani mutu wathunthu Miyambi 6