Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 5:6-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;Mayendedwe ace adzandira dzandi dzandi osadziwa iye.

7. Ndipo tsopano ana, mundimvere,Musapatuke ku mau a m'kamwa mwanga.

8. Siyanitsa njira yako kutari kwa iyeyo,Osayandikira ku khomo la nyumba yace;

9. Kuti ungapereke ulemu wako kwa ena,Ndi zaka zako kwa ankhanza;

10. Kuti mphamvu yako isakhutitse alendo,Ndi kuti usagwire nchito m'nyumba ya wacilendo;

11. Ungalire pa cimariziro cako,Pothera nyama yako ndi thupi lako;

12. Ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,Mtima wanga ndi kunyoza cidzudzulo;

13. Ndipo sindinamvera mau a aphunzitsi anga;Ngakhale kucherera makutu kwa akundilanga mwambo!

14. Ndikadakhala m'zoipa zonse,M'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.

15. Imwa madzi a m'citsime mwako,Ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako.

16. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,Ndi mitsinje ya madzi m'makwalala?

17. Ikhale ya iwe wekha,Si ya alendo okhala nawe ai.

18. Adalitsike kasupe wako;Ukondwere ndi mkazi wokula nayo.

19. Ngati mbawala yokonda ndi cinkhoma cacisomo,Maere ace akukwanire nthawi zonse;Ukodwe ndi cikondi cace osaleka.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 5