Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 5:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi waciwerewere,Ndi kufungatira cifuwa ca mkazi wacilendo?

21. Pakuti njira za munthu ziri pamaso pa Yehova,Asinkhasinkha za mayendedwe ace onse.

22. Zoipazacezacezidzagwira woipa;Adzamangidwa ndi zingwe za ucimo wace.

23. Adzafa posowa mwambo;Adzasocera popusa kwambiri.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 5