Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 5:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Imwa madzi a m'citsime mwako,Ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako.

16. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,Ndi mitsinje ya madzi m'makwalala?

17. Ikhale ya iwe wekha,Si ya alendo okhala nawe ai.

18. Adalitsike kasupe wako;Ukondwere ndi mkazi wokula nayo.

19. Ngati mbawala yokonda ndi cinkhoma cacisomo,Maere ace akukwanire nthawi zonse;Ukodwe ndi cikondi cace osaleka.

20. Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi waciwerewere,Ndi kufungatira cifuwa ca mkazi wacilendo?

21. Pakuti njira za munthu ziri pamaso pa Yehova,Asinkhasinkha za mayendedwe ace onse.

22. Zoipazacezacezidzagwira woipa;Adzamangidwa ndi zingwe za ucimo wace.

23. Adzafa posowa mwambo;Adzasocera popusa kwambiri.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 5