Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 5:12-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo,Mtima wanga ndi kunyoza cidzudzulo;

13. Ndipo sindinamvera mau a aphunzitsi anga;Ngakhale kucherera makutu kwa akundilanga mwambo!

14. Ndikadakhala m'zoipa zonse,M'kati mwa msonkhano ndi khamu la anthu.

15. Imwa madzi a m'citsime mwako,Ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako.

16. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja,Ndi mitsinje ya madzi m'makwalala?

17. Ikhale ya iwe wekha,Si ya alendo okhala nawe ai.

18. Adalitsike kasupe wako;Ukondwere ndi mkazi wokula nayo.

19. Ngati mbawala yokonda ndi cinkhoma cacisomo,Maere ace akukwanire nthawi zonse;Ukodwe ndi cikondi cace osaleka.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 5