1. Mwananga, mvera nzeru yanga;Cherera makutu ku luntha langa;
2. Ukasunge zolingalira,Milomo yako ilabadire zomwe udziwa.
3. Pakuti milomo ya mkazi waciwerewere ikukha uci;M'kamwa mwace muti see koposa mafuta.
4. Cimariziro cace ncowawa ngati civumulo,Ndi cakuthwa ngati lupanga lakuthwa konse konse.
5. Mayendedwe ace atsikira kuimfa;Mapazi ace aumirira kumanda;
6. Sasinkhasinkha bwino za njira ya moyo;Mayendedwe ace adzandira dzandi dzandi osadziwa iye.