9. Idzaika cisada ca cisomo pamtu pako;Idzakupatsa korona wokongola.
10. Tamvera mwananga, nulandire mau anga;Ndipo zaka za moyo wako zidzacuruka.
11. Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru,Ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.
12. Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;Ukathamanga, sudzapunthwa.
13. Gwira mwambo, osauleka;Uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.
14. Usalowe m'mayendedwe ocimwa,Usayende m'njira ya oipa.
15. Pewapo, osapitamo;Patukapo, nupitirire.
16. Pakuti akapanda kucita zoipa, samagona;Ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwacokera.
17. Pakuti amadya cakudya ca ucimo,Namwa vinyo wa cifwamba.
18. Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kuca,Kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.
19. Njira ya oipa ikunga mdima;Sadziwa cimene ciwapunthwitsa,
20. Mwananga, tamvera mau anga;Cherera makutu ku zonena zanga.
21. Asacoke ku maso ako;Uwasunge m'kati mwa mtima wako.
22. Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza,Nalamitsa thupi lao lonse.
23. Cinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga;Pakuti magwero a moyo aturukamo.
24. Tasiya m'kamwa mokhota,Uike patari milomo yopotoka.
25. Maso ako ayang'ane m'tsogolo,Zikope zako zipenye moongoka,
26. Sinkasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako;Njira zako zonse zikonzeke.
27. Usapatuke ku dzanja lamanja kapena kulamanzere;Suntha phazi lako kusiya zoipa.