Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 4:2-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Pakuti ndikuphunzitsani zabwino;Musasiye cilangizo canga.

3. Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga,Wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabala wina.

4. Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine,Mtima wako uumirire mau anga;Sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo.

5. Tenga nzeru, tenga luntha;Usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga;

6. Usasiye nzeru, ndipo Idzakusunga;Uikonde, idzakucinjiriza.

7. Nzeru ipambana, tatenga nzeru;M'kutenga kwako konseko utenge luntha.

8. Uilemekeze, ndipo idzakukweza;Idzakutengera ulemu pamene uifungatira.

9. Idzaika cisada ca cisomo pamtu pako;Idzakupatsa korona wokongola.

10. Tamvera mwananga, nulandire mau anga;Ndipo zaka za moyo wako zidzacuruka.

11. Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru,Ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama.

12. Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda;Ukathamanga, sudzapunthwa.

13. Gwira mwambo, osauleka;Uusunge; pakuti ndiwo moyo wako.

14. Usalowe m'mayendedwe ocimwa,Usayende m'njira ya oipa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 4