Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 4:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pakuti amadya cakudya ca ucimo,Namwa vinyo wa cifwamba.

18. Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbanda kuca,Kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.

19. Njira ya oipa ikunga mdima;Sadziwa cimene ciwapunthwitsa,

20. Mwananga, tamvera mau anga;Cherera makutu ku zonena zanga.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 4