Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 31:4-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Mafumu, Lemueli, mafumu sayenera kumwa vinyo;Akalonga sayenera kunena, Cakumwa caukali ciri kuti?

5. Kuti angamwe, naiwale malamulo,Naweruze mokhota anthu onse osautsidwa.

6. Wofuna kufa umpatse cakumwa caukali,Ndi vinyo kwa owawa mtima;

7. Amwe, narwale umphawi wace, Osakumbukiranso bvuto lace.

8. Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula,Ndi mlandu wa amasiye onse.

9. Tsegula pakamwa pako,Nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.

10. Mkazi wangwiro ndani angampeze?Pakuti mtengo wace uposa ngale.

11. Mtima wa mwamuna wace umkhulupirira,Sadzasowa phindu.

12. Mkaziyo amcitira zabwino, si zoipa,Masiku onse a moyo wace.

13. Afuna ubweya ndi thonje,Nacita mofunitsa ndi manja ace.

14. Akunga zombo za malonda;Nakatenga zakudya zace kutari.

15. Aukanso kusanace,Napatsa banja lace zakudya, nagawira adzakazi ace nchito.

16. Asinkhasinkha za munda, naugula;Naoka mipesa ndi zipatso za manja ace.

17. Amanga m'cuuno mwace ndi mphamvu,Nalimbitsa mikono yace,

Werengani mutu wathunthu Miyambi 31