Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 31:10-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mkazi wangwiro ndani angampeze?Pakuti mtengo wace uposa ngale.

11. Mtima wa mwamuna wace umkhulupirira,Sadzasowa phindu.

12. Mkaziyo amcitira zabwino, si zoipa,Masiku onse a moyo wace.

13. Afuna ubweya ndi thonje,Nacita mofunitsa ndi manja ace.

14. Akunga zombo za malonda;Nakatenga zakudya zace kutari.

15. Aukanso kusanace,Napatsa banja lace zakudya, nagawira adzakazi ace nchito.

16. Asinkhasinkha za munda, naugula;Naoka mipesa ndi zipatso za manja ace.

17. Amanga m'cuuno mwace ndi mphamvu,Nalimbitsa mikono yace,

18. Azindikira kuti malonda ace ampindulira;Nyali yace sizima usiku.

19. Agwira njinga ya thonje ndi dzanja lace,Nafumbata mtengo wace.

20. Aolowera cikhato cace osauka;Natambasulira aumphawi manja ace.

21. Saopera banja lace cipale cofewa;Pakuti banja lace lonse libvala mlangali.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 31