Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 30:9-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani?Kapena ndingasauke ndi kuba,Ndi kuchula dzina la Mulungu wanga pacabe.

10. Usanamizire kapolo kwa mbuyace,Kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.

11. Pali mbadwo wotemberera atate ao,Osadalitsa amao.

12. Pali mbadwo wodziyesa oyera,Koma osasamba litsilo lao.

13. Pali mbadwo wokwezatu maso ao,Zikope zao ndi kutukula.

14. Pali mbadwo mano ao akunga malupanga, zibwano zao zikunga mipeni;Kuti adye osauka kuwacotsa kudziko, ndi aumphawi kuwacotsa mwa anthu.

15. Msundu uli ndi ana akazi awiri ati, Patsa, patsa,Pali zinthu zitatu sizikhuta konse,Ngakhale zinai sizinena, Kwatha:

16. Manda, ndi cumba,Dziko losakhuta madzi,Ndi moto wosanena, Kwatha.

17. Diso locitira atate wace ciphwete, ndi kunyoza kumvera amace,Makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya,

Werengani mutu wathunthu Miyambi 30