28. Buluzi ungamgwire m'manja,Koma ali m'nyumba za mafumu.
29. Pali zinthu zitatu ziyenda cinya cinya;Ngakhale zinai ziyenda mwaufulu:
30. Mkango umene uposa zirombo kulimba,Supambukira cinthu ciri conse;
31. Kavalo wolimba m'cuuno, ndi tonde,Ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ace.
32. Ngati wapusa podzikweza,Ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa.
33. Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo;Ndi popsinja mpfuno, mwazi uturukamo;Ndi potimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.