2. Pakuti ndipambana anthu onse kupulukira,Ndiribe luntha la munthu.
3. Sindinaphunzira nzeruNgakhale kudziwa Woyerayo.
4. Ndani anakwera kumwamba natsikanso?Ndani wakundika nafumbata mphepo?Ndani wamanga madzi m'maraya ace?Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko?Dzina lace ndani? dzina la mwanace ndani? kapena udziwa.
5. Mau onse a Mulungu ali oyengeka;Ndiye cikopa ca iwo amene amkhulupirira.
6. Usaoniezere kanthu pa mau ace,Angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama.
7. Zinthu ziwiri ndakupemphani,Musandimane izo ndisanamwalire:
8. Mundicotsere kutari zacabe ndi mabodza;Musandipatse umphawi, ngakhale cuma,Mundidyetse zakudya zondiyenera;
9. Ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani?Kapena ndingasauke ndi kuba,Ndi kuchula dzina la Mulungu wanga pacabe.
10. Usanamizire kapolo kwa mbuyace,Kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.