17. Diso locitira atate wace ciphwete, ndi kunyoza kumvera amace,Makungubwi a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya,
18. Zinthu zitatu zindithetsa nzeru,Ngakhale zinai, sindizidziwa:
19. Njira ya mphungu m'mlengalenga,Njira ya njoka pamwala,Njira ya ngalawa pakati pa nyanja.Njira ya mwamuna ndi namwali.
20. Comweco njira ya mkazi wacigololo;Adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinacita zoipa,
21. Cifukwa ca zinthu zitatu dziko linthunthumira;Ngakhale cifukwa ca zinai silingathe kupirira nazo:
22. Cifukwa ca kapolo pamene ali mfumu;Ndi citsiru citakhuta zakudya;
23. Cifukwa ca mkazi wodedwa wokwatidwa;Ndi mdzakazi amene adzalandira colowa ca mbuyace.
24. Ziripo zinai ziri zazing'ono padziko;Koma zipambana kukhala zanzeru:
25. Nyerere ndi mtundu wosalimba,Koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe.
26. Mbira ndi mtundu wopanda mphamvu,Koma ziika nyumba zao m'matanthwe.
27. Dzombe liribe mfumu,Koma lituruka lonse mabwalo mabwalo.