Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 30:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mau a Aguri mwana wa Yake; uthenga. Munthuyo anati, Ndadzitopetsa, Mulungu;Ndadzitopetsa, Mulungu, ndathedwa;

2. Pakuti ndipambana anthu onse kupulukira,Ndiribe luntha la munthu.

3. Sindinaphunzira nzeruNgakhale kudziwa Woyerayo.

4. Ndani anakwera kumwamba natsikanso?Ndani wakundika nafumbata mphepo?Ndani wamanga madzi m'maraya ace?Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko?Dzina lace ndani? dzina la mwanace ndani? kapena udziwa.

5. Mau onse a Mulungu ali oyengeka;Ndiye cikopa ca iwo amene amkhulupirira.

6. Usaoniezere kanthu pa mau ace,Angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama.

7. Zinthu ziwiri ndakupemphani,Musandimane izo ndisanamwalire:

8. Mundicotsere kutari zacabe ndi mabodza;Musandipatse umphawi, ngakhale cuma,Mundidyetse zakudya zondiyenera;

9. Ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani?Kapena ndingasauke ndi kuba,Ndi kuchula dzina la Mulungu wanga pacabe.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 30