6. M'kulakwa kwa woipa muli msampha;Koma wolungama ayimba, nakondwera.
7. Wolungama asamalira mlandu wa osauka;Koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.
8. Anthu onyoza atentha mudzi;Koma anzeru alezetsa mkwiyo.
9. Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa,Ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.
10. Anthu ankhanza ada wangwiro;Koma oongoka mtima asamalira moyowace.
11. Citsiru cibvumbulutsa mkwiyo wace wonse;Koma wanzeru auletsa nautontholetsa.
12. Mkuru akamvera cinyengo,Atumuki ace onse ali oipa,
13. Waumphawi ndi wotsendereza akumana;Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo.
14. Mfumu yolamulira osauka mwantheradi,Mpando wace udzakhazikika kufikira nthawi zonse.
15. Ntyole ndi cidzudzulo zipatsa nzeru;Koma mwana womlekerera acititsa amace manyazi.