Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 29:13-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Waumphawi ndi wotsendereza akumana;Yehova apenyetsa maso a onse awiriwo.

14. Mfumu yolamulira osauka mwantheradi,Mpando wace udzakhazikika kufikira nthawi zonse.

15. Ntyole ndi cidzudzulo zipatsa nzeru;Koma mwana womlekerera acititsa amace manyazi.

16. Pocuruka oipa zolakwa zicuruka;Koma olungama adzaona kugwa kwao.

17. Langiza mwana wako, ndipo adzakupumitsa;Nadzasangalatsa moyo wako.

18. Popanda cibvumbulutso anthu amasauka;Koma wosunga cilamulo adalitsika.

19. Kapolo sangalangizidwe ndi mau,Pakuti azindikira koma osabvomera.

20. Kodi uona munthu wansontho m'mau ace?Ngakhale citsiru cidzacenjera, koma ameneyo ai.

21. Yemwe alera kapolo wace mwa ufulu kuyambira ubwana wace,Pambuyo pace adzadziyesa mwana wobala.

22. Mwamuna wamkwiyo aputa makangano;Waukali acuruka zolakwa.

23. Kudzikuza kwa munthu kudzamcepetsa;Koma wokhala ndi mtima wodzicepetsa adzalemekezedwa.

24. Woyenda ndi mbala ada moyo wace wace;Amva kulumbira, koma osaulula kanthu.

25. Kuopa anthu kuchera msampha;Koma wokhulupirira Yehova adzapulumuka,

Werengani mutu wathunthu Miyambi 29