1. Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri,Adzasweka modzidzimuka, palibe comciritsa.
2. Pocuruka olungama anthu akondwa;Koma polamulira woipa anthu ausa moyo.
3. Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wace;Koma wotsagana ndi akazi adama amwaza cuma.
4. Mfumu akhazikitsa dziko ndi ciweruzo;Koma wosonkhetsa anthu mphatso alipululutsa.
5. Wosyasyalika mnzace Acherera mapazi ace ukonde.
6. M'kulakwa kwa woipa muli msampha;Koma wolungama ayimba, nakondwera.
7. Wolungama asamalira mlandu wa osauka;Koma woipa alibe nzeru yakuudziwa.
8. Anthu onyoza atentha mudzi;Koma anzeru alezetsa mkwiyo.
9. Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa,Ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.
10. Anthu ankhanza ada wangwiro;Koma oongoka mtima asamalira moyowace.