Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 28:15-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Monga mkango wobangula ndi cirombo coyendayenda,Momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.

16. Kalonga wosowa nzeru apambana kusautsa;Koma yemwe ada cisiriro adzatanimphitsa moyo wace.

17. Woparamula mlandu wakupha munthu adzathawira kudzenje;Asamuletse.

18. Woyenda mwangwiro adzapulumuka;Koma wokhota m'mayendedwe ace adzagwa posacedwa.

19. Wolima munda wace zakudya zidzamkwanira;Koma wotsata anthu opanda pace umphawi udzamkwanira.

20. Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri;Koma wokangaza kulemera sadzapulumuka cilango,

21. Cetera siliri labwino,Ngakhale kulakwa kuti ukadye kanthu.

22. Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera,Osadziwa kuti umphawi udzamfikira.

23. Adzamkomera mtima wodzudzula m'tsogolo mwace,Koposa wosyasyalika ndi lilime lace.

24. Wobera atate wace, pena amace, nati, Palibe kulakwa;Ndiye mnzace wa munthu wopasula.

25. Wodukidwa mtima aputa makangano;Koma wokhulupirira Yehova adzakula.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 28