23. Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji,Samalira magulu ako;
24. Pakuti cuma siciri cosatha;Kodi korona alipobe mpaka mibadwo mibadwo?
25. Amatuta maudzu, msipu uoneka,Achera masamba a kumapiri,
26. Ana a nkhosa akubveka,Atonde aombolera munda;
27. Mkaka wa mbuzi udzakukwanira kudya;Ndi a pa banja lako ndi adzakazi ako.