Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 27:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Yemwe adalitsa mnzace ndi mau akuru pouka mamawa,Anthu adzaciyesa cimeneco temberero.

15. Kudonthadontha tsiku lamvula,Ndi mkazi wolongolola ali amodzimodzi.

16. Wofuna kumletsayo afuna kuletsa mphepo;Dzanja lace lamanja lingogwira mafuta.

17. Citsulo cinola citsulo;Comweco munthu anola nkhope ya mnzace.

18. Wosunga mkuyu adzadya zipatso zace;Wosamalira ambuyace adzalemekezedwa.

19. Monga m'madzi nkhope zionana,Momwemo mitima ya anthu idziwana.

20. Kunsi kwa manda ndi kucionongeko sikukhuta;Ngakhale maso a munthu sakhutai.

21. Siliva asungunuka m'mbiya,Ndi golidi m'ng'anjo,Motero comwe munthu acitama adziwika naco.

22. Ungakhaleukonolacitsirum'mtondo ndi munsi, pamodzi ndi mphale,Koma utsiru wace sudzamcoka.

23. Udziwitsitse zoweta zako ziri bwanji,Samalira magulu ako;

24. Pakuti cuma siciri cosatha;Kodi korona alipobe mpaka mibadwo mibadwo?

Werengani mutu wathunthu Miyambi 27