Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 26:18-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Monga woyaruka woponya nsakali,Mibvi, ndi imfa,

19. Momwemo wonyenga mnzace ndi kuti, Ndi kusewera kumeneku.

20. Posowa nkhuni moto ungozima;Ndi popanda kazitape makangano angoleka.

21. Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto;Momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.

22. Mau a kazitape ndi zakudya zolongosokaZitsikira m'kati mwa mimba.

23. Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipaIkunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva.

24. Wakuda mnzace amanyenga ndi milomo yace;Koma akundika cinyengo m'kati mwace;

25. Pamene akometsa mau ace usamkhulupirire;Pakuti m'mtima mwace muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.

26. Angakhale abisa udani wace pocenjera,Koma udio wace udzabvumbulutsidwa posonkhana anthu.

27. Wokumba dzenje adzagwamo,Wogubuduza mwala, udzabweranso pa iye mwini.

28. Lilime lonama lida omwewo linawasautsa;Ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 26