18. Monga woyaruka woponya nsakali,Mibvi, ndi imfa,
19. Momwemo wonyenga mnzace ndi kuti, Ndi kusewera kumeneku.
20. Posowa nkhuni moto ungozima;Ndi popanda kazitape makangano angoleka.
21. Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto;Momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.
22. Mau a kazitape ndi zakudya zolongosokaZitsikira m'kati mwa mimba.
23. Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipaIkunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva.
24. Wakuda mnzace amanyenga ndi milomo yace;Koma akundika cinyengo m'kati mwace;
25. Pamene akometsa mau ace usamkhulupirire;Pakuti m'mtima mwace muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
26. Angakhale abisa udani wace pocenjera,Koma udio wace udzabvumbulutsidwa posonkhana anthu.