Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 26:12-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru?Ngakhale citsiru cidzacenjera koma ameneyo ai.

13. Wolesi ati, Mkango uli panjira,Wobangulawo uli m'makwalala.

14. Monga citseko cikankhikira pa zitsulo za pamphuthu,Momwemo wolesi agubuduka pakama pace.

15. Wolesi alonga dzanja lace m'mbale;Kumtopetsa kulibweza kukamwa kwace.

16. Wolesi adziyesa wanzeruKoposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira.

17. Wakungopita ndi kubvutika ndi ndeu yosakhala yaceAkunga wogwira makutu a garu.

18. Monga woyaruka woponya nsakali,Mibvi, ndi imfa,

19. Momwemo wonyenga mnzace ndi kuti, Ndi kusewera kumeneku.

20. Posowa nkhuni moto ungozima;Ndi popanda kazitape makangano angoleka.

21. Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto;Momwemo munthu wamakangano autsa ndeu.

22. Mau a kazitape ndi zakudya zolongosokaZitsikira m'kati mwa mimba.

23. Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipaIkunga mbale yadothi anaimata ndi mphala yasiliva.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 26