Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 26:1-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Monga cipale cofewa m'malimwe, ndi mvula m'masika,Momwemo ulemu suyenera citsiru.

2. Monga mpheta irikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka,Momwemo temberero la pacabe silifikira.

3. Cikoti ciyenera kavalo, ndi cam'kamwa ciyenera buru,Ndi ntyole iyenera pamsana pa zitsiru.

4. Usayankhe citsiru monga mwa utsiru wace,Kuti ungafanane naco iwe wekha.

5. Yankha citsiru monga mwa utsiru wace,Kuti asadziyese wanzeru.

6. Wotumiza mau ndi dzanja la citsiruAdula mapazi ace, namwa zompweteka.

7. Miyendo ya wopunduka iri yolobodoka,Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.

8. Monga thumba la ngale m'mulu wa miyala,Momwemo wocitira citsiru ulemu.

9. Monga munga wolasa dzanja la woledzera,Momwemo mwambi m'kamwa mwa zitsiru.

10. Monga woponya mibvi ndi kulasa onse,Momwemo wolembera citsiru, ndi wolembera omwe alikupita panjira.

11. Monga garu abweranso ku masanzi ace,Momwemo citsiru cicitanso zopusa zace.

12. Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru?Ngakhale citsiru cidzacenjera koma ameneyo ai.

13. Wolesi ati, Mkango uli panjira,Wobangulawo uli m'makwalala.

14. Monga citseko cikankhikira pa zitsulo za pamphuthu,Momwemo wolesi agubuduka pakama pace.

15. Wolesi alonga dzanja lace m'mbale;Kumtopetsa kulibweza kukamwa kwace.

16. Wolesi adziyesa wanzeruKoposa anthu asanu ndi awiri akuyankha mozindikira.

17. Wakungopita ndi kubvutika ndi ndeu yosakhala yaceAkunga wogwira makutu a garu.

18. Monga woyaruka woponya nsakali,Mibvi, ndi imfa,

Werengani mutu wathunthu Miyambi 26