4. Cotsera siliva mphala yace,Mmisiri wa ng'anjo aturutsamo mbale;
5. Cotsera woipa pamaso pa mfumu,Mpando wace udzakhazikika m'cilungamo.
6. Usadzitame pamaso pa mfumu,Ngakhale kuima m'malo mwa akuru;
7. Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno,Kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga,Amene maso ako anamuona.
8. Usaturuke mwansontho kukalimbana,Ungalephere pa kutha kwace,Atakucititsa mnzako manyazi.
9. Nena mlandu wako ndi mnzako,Osaulula zinsinsi za mwini;
10. Kuti wakumva angakutonze,Mbiri yako yoipa ndi kusacoka.