Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 23:31-35 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

31. Usayang'ane pavinyo alikufiira.Alikung'azimira m'cikho.Namweka mosalala.

32. Pa citsiriziro cace aluma ngati njoka,Najompha ngati mamba.

33. Maso ako adzaona zacilendo,Mtima wako udzalankhula zokhota.

34. Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja,Pena wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalawa.

35. Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine;Anandikwapula, osamva ine;Ndidzauka nthawi yanji? Ndidzafuna-funanso vinyoyo.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 23