Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 23:17-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Mtima wako usacitire nsanje akucimwawo;Koma opabe Yehova tsiku lonse;

18. Pakutitu padzakhala mphotho;Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.

19. Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru,Ulunjikitse mtima wako m'njiramo.

20. Usakhale mwa akumwaimwa vinyo,Ndi ankhuli osusuka.

21. Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka;Ndipo kusinza kudzabveka munthu nsanza.

22. Tamvera atate wako anakubala,Usapeputse amako atakalamba.

23. Gula ntheradi, osaigulitsa;Nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.

24. Atate wa wolungama adzasekeradi;Wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.

25. Atate wako ndi amako akondwere,Amako wakukubala asekere.

26. Mwananga, undipatse mtima wako,Maso ako akondwere ndi njira zanga,

27. Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya;Ndipo mkazi waciwerewere ndiye mbuna yopapatiza.

28. Pakuti abisalira ngati wacifwamba,Nacurukitsa anthu a ciwembu.

29. Ndani ali ndi cisoni? ndani asauka? ndani ali ndi makangano?Ndani ang'ung'udza? ndani alasidwa cabe? ndani afiira maso?

30. Ngamene acedwa pali vinyo,Napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa.

31. Usayang'ane pavinyo alikufiira.Alikung'azimira m'cikho.Namweka mosalala.

32. Pa citsiriziro cace aluma ngati njoka,Najompha ngati mamba.

33. Maso ako adzaona zacilendo,Mtima wako udzalankhula zokhota.

34. Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja,Pena wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalawa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 23