10. Usasunthe cidziwitso cakale ca m'malire;Ngakhale kulowa m'minda ya amasiye;
11. Pakuti Mombolo wao walimba;Adzawanenera mlandu wao pa iwe.
12. Lozetsa mtima wako kumwambo,Ndi makutu ako ku mau a nzeru.
13. Usamane mwana cilango;Pakuti ukammenya ndi ntyole safa ai.
14. Udzammenya ndi ntyole,Nudzapulumutsa moyo wace kunsi kwa manda.
15. Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru,Mtima wanga wa inedi udzakondwa;
16. Imso zanga zidzasangalala,Polankhula milomo yako zoongoka.
17. Mtima wako usacitire nsanje akucimwawo;Koma opabe Yehova tsiku lonse;
18. Pakutitu padzakhala mphotho;Ndipo ciyembekezo cako sicidzalephereka.