1. Pamene ukhala ulinkudya ndi mkuru,Zikumbukira ameneyo ali pamaso pako;
2. Nuike mpeni pakhosi pako,Ngati uli wadyera.
3. Usakhumbe zolongosoka zace;Pokhala zakudya zonyenga.
4. Usadzitopetse kuti ulemere;Leka nzeru yako yako.
5. Kodi upenyeranji cimene kulibe?Pakuti cuma cunera mapiko,Ngati mphungu youluka mumlengalenga.
6. Usadye zakudya zace za wa maso ankhwenzule,Ngakhale kukhumba zolongosoka zace;
7. Pakuti monga asinkha m'kati mwace, ali wotere;Ati kwa iwe, Idya numwe;Koma mtima wace suli pa iwe.
8. Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza,Ndi kutaya mau ako okondweretsa.
9. Usalankhule m'makutu a wopusa;Pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako.