7. Wolemera alamulira osauka;Ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.
8. Wofesa zosalungama adzakolola tsoka;Ndipo ntyole ya mkwiyo wace idzalephera.
9. Mwini diso lamataya adzadala;Pakuti apatsa osauka zakudya zace.
10. Ukainga wonyoza, makangano adzaturuka;Makani ndi manyazi adzalekeka.
11. Wokonda kuyera mtima,Mfumu idzakhala bwenzi lace cifukwa ca cisomo ca milomo yace.
12. Maso a Yehova acinjiriza wodziwa;Koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.
13. Waulesi ati, Pali mkango panjapo,Ndidzaphedwa pamakwalalapo.
14. M'kamwa mwa mkazi waciwerewere muli dzenje lakuya;Yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.
15. Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana;Koma ntyole yomlangira idzauingitsira kutari.
16. Wotsendereza waumphawi kuti acurukitse cuma cace,Ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.
17. Chera makutu ako, numvere mau a anzeru,Nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.
18. Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako,Ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.
19. Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi,Kuti ukhulupirire Yehova.