Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 22:18-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako,Ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.

19. Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi,Kuti ukhulupirire Yehova.

20. Kodi sindinakulembera zoposa Za uphungu ndi nzeru;

21. Kuti ukadziwitse ntheradi yace ya mau oona,Nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?

22. Usalande za waumphawi cifukwa ali waumphawi,Ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo.

23. Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao;Omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.

24. Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga;Ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;

25. Kuti ungaphunzire mayendedwe ace,Ndi kutengera moyo wako msampha,

26. Usakhale wodulirana mpherere,Ngakhale kumperekera cikole ca ngongole zace.

27. Ngati ulibe cobwezeraKodi acotserenji kama lako pansi pako?

28. Usasunthe cidziwitso cakale ca m'malire,Cimene makolo ako anaciimika.

29. Kodi upenya munthu wofulumiza nchito zace?Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu acabe.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 22