1. Mbiri yabwino ifunika kopambana cuma cambiri;Kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golidi.
2. Wolemera ndi wosauka akumana,Wolenga onsewo ndiye Yehova.
3. Wocenjera aona zoipa, nabisala;Koma acibwana angopitirira, nalipitsidwa.
4. Mphotho ya cifatso ndi kuopa, YehovaNdiye cuma, ndi ulemu, ndi moyo.
5. Minga ndi misampha iri m'njira ya wokhota;Koma wosunga moyo wace adzatarikira imeneyo.
6. Phunzitsa mwana poyamba njira yace;Ndipo angakhale atakalamba sadzacokamo.
7. Wolemera alamulira osauka;Ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.
8. Wofesa zosalungama adzakolola tsoka;Ndipo ntyole ya mkwiyo wace idzalephera.
9. Mwini diso lamataya adzadala;Pakuti apatsa osauka zakudya zace.
10. Ukainga wonyoza, makangano adzaturuka;Makani ndi manyazi adzalekeka.
11. Wokonda kuyera mtima,Mfumu idzakhala bwenzi lace cifukwa ca cisomo ca milomo yace.