3. Kucita cilungamo ndi ciweruzoKupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.
4. Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,Ndi nyali ya oipa, ziri cimo.
5. Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu;Koma yense wansontho angopeza umphawi.
6. Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.
7. Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola;Cifukwa akana kucita ciweruzo.
8. Wosenza cimo njira yace ikhotakhota;Koma nchito ya woyera mtima ilungama.
9. Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
10. Wamphulupulu mtima wace umkhumba zoipa;Sakomera mtima mnzace.
11. Polangidwa wonyoza, wacibwana alandira nzeru,Naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.
12. Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu,Kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.