24. Wonyada wodzikuza dzina lace ndiye wonyoza;Acita mwaukali modzitama.
25. Cifuniro ca wolesi cimupha;Cifukwa manja ace akana kugwira nchito.
26. Ena asirira modukidwa tsiku lonse;Koma wolungama amapatsa osamana.
27. Nsembe ya oipa inyansa;Makamaka pakudza nayo iwo mwaciwembu.
28. Mboni yonama idzafa;Koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika,
29. Munthu woipa aumitsa nkhope yace;Koma woongoka mtima akonza njira zace.
30. Kulibe nzeru ngakhale lunthaNgakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.
31. Kavalo amakonzedweratu cifukwa ca tsiku la nkhondo;Koma wopulumutsa ndiye Yehova.