Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 21:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;Koma wopusa angozimeza.

21. Wolondola cilungamo ndi cifundoApeza moyo, ndi cilungamo, ndi ulemu.

22. Wanzeru akwera pa mudzi wa olimba,Nagwetsa mphamvu yace imene anaikhulupirira.

23. Wosunga m'kamwa mwace ndi lilime laceAsunga moyo wace kumabvuto.

24. Wonyada wodzikuza dzina lace ndiye wonyoza;Acita mwaukali modzitama.

25. Cifuniro ca wolesi cimupha;Cifukwa manja ace akana kugwira nchito.

26. Ena asirira modukidwa tsiku lonse;Koma wolungama amapatsa osamana.

27. Nsembe ya oipa inyansa;Makamaka pakudza nayo iwo mwaciwembu.

28. Mboni yonama idzafa;Koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika,

29. Munthu woipa aumitsa nkhope yace;Koma woongoka mtima akonza njira zace.

30. Kulibe nzeru ngakhale lunthaNgakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.

31. Kavalo amakonzedweratu cifukwa ca tsiku la nkhondo;Koma wopulumutsa ndiye Yehova.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 21