Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 21:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi;Aulozetsa komwe afuna.

2. Njira zonse za munthu zilungama pamaso pace;Koma Yehova ayesa mitima.

3. Kucita cilungamo ndi ciweruzoKupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

4. Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,Ndi nyali ya oipa, ziri cimo.

5. Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu;Koma yense wansontho angopeza umphawi.

6. Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

7. Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola;Cifukwa akana kucita ciweruzo.

8. Wosenza cimo njira yace ikhotakhota;Koma nchito ya woyera mtima ilungama.

9. Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.

10. Wamphulupulu mtima wace umkhumba zoipa;Sakomera mtima mnzace.

11. Polangidwa wonyoza, wacibwana alandira nzeru,Naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.

12. Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu,Kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.

13. Wotseka makutu ace polira waumphawi,Nayenso adzalira koma osamvedwa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 21