1. Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi;Aulozetsa komwe afuna.
2. Njira zonse za munthu zilungama pamaso pace;Koma Yehova ayesa mitima.
3. Kucita cilungamo ndi ciweruzoKupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.
4. Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,Ndi nyali ya oipa, ziri cimo.
5. Zoganizira za wakhama zicurukitsadi katundu;Koma yense wansontho angopeza umphawi.
6. Kupata cuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.
7. Ciwawa ca amphulupulu cidzawakokolola;Cifukwa akana kucita ciweruzo.
8. Wosenza cimo njira yace ikhotakhota;Koma nchito ya woyera mtima ilungama.
9. Kukhala pa ngondya ya tsindwi kufunikaKuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.
10. Wamphulupulu mtima wace umkhumba zoipa;Sakomera mtima mnzace.