Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 20:9-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga,Ndayera opanda cimo?

10. Miyeso yosiyana, ndi malicero osiyana,Zonse ziwirizi zinyansa Yehova.

11. Ngakhale mwana adziwika ndi nchito zace;Ngati nchito yace iri yoyera ngakhale yolungama.

12. Khutu lakumva, ndi diso lopenya,Yehova anapanga onse awiriwo.

13. Usakonde tulo ungasauke;Phenyula maso, udzakhuta zakudya.

14. Wogula ati, Cacabe cimeneco.Koma atacoka adzitama.

15. Alipo golidi ndi ngale zambiri;Koma milomo yodziwa ndiyo cokometsera ca mtengo wapatari.

16. Tenga maraya a woperekera mlendo cikole;Woperekera mkazi wacilendo cikole umgwire mwini.

17. Zakudya za cinyengo zikondweretsa munthu;Koma pambuyo pace m'kamwa mwace mudzadzala tinsangalabwi.

18. Uphungu utsimikiza zolingalira,Ponya nkhondo utapanga upo.

19. Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi;Usadudukire woyasama milomo yace.

20. Wotemberera atate wace ndi, amace,Nyali yace idzazima mu mdima woti bi.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 20