Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 20:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Vinyo acita ciphwete, cakumwa caukali cisokosa;Wosocera nazo alibe nzeru.

2. Kuopsya kwa mfumu ndiko kubangula kwa mkango;Womputa acimwira moyo wace wace.

3. Kuli ulemu kwa mwamuna kupewa ndeu;Koma zitsiru zonse zimangokangana,

4. Wolesi salima cifukwa ca cisanu;Adzapemphapempha m'masika osalandira kanthu.

5. Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya;Koma munthu wozindikira adzatungapo,

6. Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwace;Koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?

7. Wolungama woyenda mwangwiro,Anace adala pambuyo pace.

8. Mfumu yokhala pa mpando waweruziraIpitikitsa zoipa zonse ndi maso ace.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 20