20. Tamvera uphungu, nulandire mwambo,Kuti ukhale wanzeru pa cimariziro cako,
21. Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu;Koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.
22. Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace;Ndipo wosauka apambana munthu wonama.
23. Kuopa Yehova kupatsa moyo;Wokhala nako adzakhala wokhuta;Zoipa sizidzamgwera.
24. Wolesi alonga dzanja lace m'mbale,Osalibwezanso kukamwa kwace.
25. Menya wonyoza, ndipo acibwana adzaceniera;Nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.
26. Wolanda za atate, ndi wopitikitsa amai,Ndiye mwana wocititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.