Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Miyambi 19:17-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Wocitira waumphawi cifundo abwereka Yehova;Adzambwezera cokoma caceco.

18. Menya mwanako, ciyembekezero ciripo,Osafunitsa kumuononga.

19. Munthu waukali alipire mwini;Pakuti ukampulumutsa udzateronso.

20. Tamvera uphungu, nulandire mwambo,Kuti ukhale wanzeru pa cimariziro cako,

21. Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu;Koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.

22. Cotikondetsa munthu ndico kukoma mtima kwace;Ndipo wosauka apambana munthu wonama.

23. Kuopa Yehova kupatsa moyo;Wokhala nako adzakhala wokhuta;Zoipa sizidzamgwera.

24. Wolesi alonga dzanja lace m'mbale,Osalibwezanso kukamwa kwace.

25. Menya wonyoza, ndipo acibwana adzaceniera;Nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.

26. Wolanda za atate, ndi wopitikitsa amai,Ndiye mwana wocititsa manyazi ndi wogwetsa nkhope.

27. Ukangofuna, mwananga, kusocera kusiya mau akudziwitsa,Leka kumva mwambo.

28. Mboni yopanda pace inyoza ciweruzo;M'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa,

29. Akonzera onyoza ciweruzo,Ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.

Werengani mutu wathunthu Miyambi 19